GOD'S VOICE

GOD'S VOICE Preaching and help people spiritually

25/03/2023

Yehovah mwini zolengedwa zonse,atamaliza kulenga chirichonse,adati tipange munthu muchifaniziro chathu ndipo adati ziribwino.
Eya okondedwa mwa khristu Yesu, inuyo ndiine,ndiife zolengedwa zake ndipo ndubwerezanso kunena kuti"ziribwino ndimoyo wathu"
Atate,
Tikupempha musatisiye tokha,tikumbutseni Kuti kwainu nkomwe tipeza mtendere weniweni.Amen

24/03/2023

Tisaiwale ndipo nthawi zonse tisamaiwale Kuti Yehovah wamoyo anatumiza khristu Yesu mwana yekhayo okondedwa padziko lapansi kuzatiombola Ife nkutiika pamalo poyenera Kuti pakukhulupirira mwaiye tisakataike koma Kuti titembenuke mtima Kuti pakutha pake pamoyo wuno tikaimbe Oyera muufumu wake kwamuyaya.
Yehovah wamoyo adalitse onse okhulupirira nabweza chotaikacho.
Amen

24/03/2023

Kumvetsera mau a Yehovah wamoyo,nkuchita chifuniro chake,zimabweretsa chimwemwe mmitima ndinso timakhala paubwenzi olimba ndi Iye wakulenga ifeyo.
Mwazuka bwanji okondedwa mwa khristu Yesu?

23/03/2023

Tizipereke kwa Yehovah wamoyo, Kuti tikhale nao maonekedwe enieni a kulambira osati kuthupi kokha,mumtimaso.
Atate, tithandizeni patokha sitingathe.
Khristu Yesu, anafera machimo athu.Tirape.

23/03/2023

Kukacha chomwechi,kumazutsana molimbikitsana zimachita bwino.
Mulungu dalitsani aliyense akuwerenga uthenga uwu nachita chifuniro chanu,muikeni pa mulingo wina, tikupempha musatisiye tokha.Amen

20/03/2023

Chimene Yehovah akufuna paife,ndichoti"TIRAPE NTHAWI ISANAFOKE KU MAPETO"
tisakondwere kwambiri pokhala ndimoyo lero,tikonze mitima yathu pakubwerera kwa Yehovah wamoyo.
Mwazi wa khristu Yesu,udaombola ife kuutchimo ndiimfa.Amen

18/03/2023

Moto umapita komwe kwasala tchire!!
Mwaswera bwanji okondedwa mwa khristu Yesu?
Tikumbusane kuti pachirichonse chomwe timachita, tizalandira mphotho yake.
Makolo,ana abale komanso anansi athu ambiri apita.
Sitikudziwa mwina ndimmene zimayenera kukhalira paulendo wao ochoka pano padziko lapansi.Mizimu yao ikautse mumtendere.
Koma funso nkumati munthu amene wamwalira ali osalungama,autsa bwanji mumtendere?
Tasala ndiiwe ndiine.Chonde tirape nthawi yatha chonde.
Utsiku wopambana komanso wamayankho.
Amen

17/03/2023

Tsiku Lina laza mmiyoyo mwathu.
Atate mupitirize ntchito yaikulu yomwe mukuchita paife nthawi zonse.
Tonthozani amitima yotsweka nimuzuzula onse akuyenda munjira zokhota kuti abwerere kwainu msanga lisanalire lipenga lotsiriza.
Dalitsani onse otikonda tetezani dziko lathu,
Abale komanso alongo anga mwa khristu Yesu,Kwacha bwanji lero?
Osasiya kupemphera pakuti woyipayo afunitsitsa tonse titasiya kutumikira yehovah wamoyo.Amen

16/03/2023

Chabwino,
Tizaiwala bwanji?
Abale,anansi,makolo,ana,omwe anali mthunzi panthawi yazuwa eya adali ndimalingaliro ambiri mmoyo wuno Koma ndithu kwamphindi,padali mudzi apa koma onse wapita ndimadzi.Tiziti chani? ulemelero ndimatamando zikhalebe kwaiye wotilengayo pakuti salakwitsa ndipo sadalakwitsepo . konse tiri munthawi Yino,tingoti Ambuye alemekezeke pakuti sikuthekera kwathu kupezeka lero ndimoyo.
Atate, tikupempha,musatisiye chomwechi,yankhulani ndimiyoyo yathu nthawi zonse.
Mwa khristu Yesu,Amen

16/03/2023

Kwacha bwanji lero konse muli mnthawi yino?
Mchirichonse tiyamika mwini chirengedwe pakuti patokha sitikanakwanitsa kumvanso mbalame zikuimba kuthokoza Iye wakulenga ifeyo pozipatsa Moyo mutsiku ili.
Tipempha chitetezo zisomo ndinso zifundo zochokera kwa Yehovah wamoyo, zisachoke paife nthawi zonse.
Atate tikuti chitani nafe mwakufuna kwainu,tirimbikitseni tisachoke painu.
Khunzani ndizanja lanu lamphamvu onse akuzunzika ndinyengo zosiyanasiyana nimuwapataa mtima wachiyembekezo onse akutsweka mtima.
Tetezani dziko lathu,mudzina wathu,banja lathu.Mwa khristu Yesu opachikidwa pamtanda kuombola ife,tapempha,Amen

Address

Neethleng Street Amersfoort
Amersfoort

Telephone

+27780812034

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when GOD'S VOICE posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Organization

Send a message to GOD'S VOICE:

Shortcuts

Share