UTM Youth Achievers 2030 Project

UTM Youth Achievers 2030 Project Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from UTM Youth Achievers 2030 Project, zomba, Zomba.

National UTM Youth Achievers is an organization which is under United Transformation Movement political organization founded by Dr Saulos Klaus Chilima, the vice president of Malawi.

Munthuyu ndamupeza , ndacheza naye ndipo wapereka chidwi kwambiri. Akudziwa zambiri za vision ya UTM. Munthuyu amapanga ...
22/07/2026

Munthuyu ndamupeza , ndacheza naye ndipo wapereka chidwi kwambiri. Akudziwa zambiri za vision ya UTM. Munthuyu amapanga kabaza ndiye ndimati timugulire Njinga yamoto . A UTM anzanga omwe mukumva mu mtimamo ngati ine tiyeni tikambilane ku inbox kuti tione kuti tipanga bwanji .

Mwadzuka bwanji abale anga a UTM party. Dzulo tinakwanitsa kusonkha K1,026,000 ndipo mmawa wa lero ndinapita ku shop kukaona njinga.
Mwachisomo cha Ambuye ogulitsa atichotsela ntengo kuchoka pa K2,950,000 kufika pa K2,850,000. Chotelo, tapereka deposit ndalama yonse yomwe mwapereka dzulo ndipo tatsala ndi balance ya K1,824,000. Ndipezeni ku Inbox , omwe mukufuna kuponya . Ambuye akudalitseni .

Chinthu ichi achiyambisa ndi a Hon Felix Ndawala. Tiyeni tigwirane nawo manja.

14/07/2026

A Chidanti atuluka chipani cha UTM. Zambiri tikupasirani

Mtsogoleri wa chipani cha *UTM Dr Dalitso Kabambe* kuyala nkhata pa maliro *a Mrs Lovely Kamanga* , mayi awo a mama Kany...
09/07/2026

Mtsogoleri wa chipani cha *UTM Dr Dalitso Kabambe* kuyala nkhata pa maliro *a Mrs Lovely Kamanga* , mayi awo a mama Kanyasko a chipani cha *UTM ku Usisya m'boma la Nkhatabay* lero pa *9* *July 2026.*

Anthu ambiri akumuyamikira mtsogoleriyu chifukwa cha mtima wake wokhala limodzi ndi anthu mu nyengo zonse zimene akukumana nazo.

Mtsogoleri azikhala wa chikondi ndi anthu. Uyudi ndi bwenzi losawona nyengo.

02/07/2026

*KAYA LERO NDE TIMVA KUYI AKWEZA CHANI ABOMAWA?😭😭*

Moyo wafika powawa muchaka choyamba cha ulamuliro wa *DPP*. Panopa zafika poti anthu tikadzuka tumathamangira pà social media kukawona chomwe boma lakweza.

Moyo wafika poti ukamapita kokagula zinthu, sukumakhala sure ngati ndalama watengayo itakakwanedi. Tabweleranso mwakale munthawi ya *MCP* imene zinthu zimangokwela daily.

*AKABAMBE anatiuza kuti kuvoteranso DPP kapena MCP ndikufuna kuti tizakhaulenso. Mawu a anthu anzeru amakomadi akagonera ndipo M'MALAWI aliyense akumbukano zomwe AKABAMBE anatichenjeza mu 2025 nthawi ya campaign 🤦‍♂️🙆‍♂️*

Ndithu Amalawi apapa nde tikukhaula zenizeni ndipo izi sizomwe timkayembekezera mwa *APM ndi DPP.* Timkayesa moyo usintha motikomera koma AYI ndithu ukupitilirabe kutiwawira.

*_AMALAWI 2030 dzavoteni mwanzeru ndipo dzalemekezeni vote yanu posankha AKABAMBE ACHIPANI CHA UTM kukhala president wadzikoli._*

DK 2030 ndiye TSOGOLO lathu LOWALA komanso moyo wokomera aliyense

* 2030 PROJECT #*

Ngati unachezapo ndi akulu awa ukhoza kunditsimikizira kuti  mwa iwo muli zinthu izi ;1- Chikondi 2- umunthu3- kuopa Mul...
25/05/2026

Ngati unachezapo ndi akulu awa ukhoza kunditsimikizira kuti mwa iwo muli zinthu izi ;

1- Chikondi
2- umunthu
3- kuopa Mulungu
4- Luntha
5- kuzichepetsa
5- Chitukuko
7-kupilira ndi kusabwenzera choipa .

Ladies and Gentlemen uyu ndi NTCHANA ndipo ndi MP kudera lathu la Blantyre Soche-Zingwangwa Constituency.

Ambiri kuderaku tikumafunsana kuti kodi uyu si mpulumutsi olonjezedwa uja ?
Fredokiss

*AMALWI KULIRA SIKUDZATHA CHIFUKWA CHA MTSOGOLERI UYU CHILIMA AMENE ANALIMBA MTIMA KUTI ASINTHE MALAWI*Ndizowonadi kuti ...
22/05/2026

*AMALWI KULIRA SIKUDZATHA CHIFUKWA CHA MTSOGOLERI UYU CHILIMA AMENE ANALIMBA MTIMA KUTI ASINTHE MALAWI*

Ndizowonadi kuti nthawi zambiri anthu oipa amadana ndi anthu abwino komanso akufuna kwabwino. *Late DR. SAULOS CHILIMA* anali munthu amene anasintha kachitidwe kandale m'dziko muno. Ena mwa inu m***a kuvomeleza kuti munayamba kutsata ndale komanso kumapita mmisonkhano ya ndale chifukwa cha *ACHILIMA.*

*Pa 10 June mma 10 AM, mmene zimkamveka kuti ndege imene inanyamula ACHILIMA yasowa, anthu ochuluka mdziko muno timkangoti ndinthabwala zap social media chabe ndipo ACHILIMA alipo. Zachisoni pa 11 June ndipomwe zinatsimikizika kuti ACHILIMA ndi anthu ena 8 amwalira pa ngozi ya ndege. Izi zinadzetsa gap yayikulu kwambiri ku dziko komanso kuchipani cha UTM.*

Pa *13 June* chaka chino, kuli mwambo okumbukira mzimu wa *ACHILIMA ndipo mwambowu uzachitikira ku Ntcheu Stadium.* Tiyeni mogwilizana ndi mtsogoleri wachipani cha *UTM wolemekezeka DR. DALITSO KABAMBE* , tidzapiteko mwaunyinji
*Continue RIP SKC*

21/05/2026

Asilikali a gulu la nkhondo la MDF ati anadula mbali zina za ndege yomwe inachita ngozi ku chikangawa pa 10 June, 2024 kuti akwanitse kunyamula bwino zidutswazo kupita nazo ku Zomba Air Base.

Izi anafotokoza pomwe komiti ya ku nyumba ya malamulo yomwe ikufufuza nkhaniyi yadabwa kuti zidutswa zomwe zili pa malowa zikusiyana ndi zomwe zinaoneka pa malo angozi.

Komitiyi motsogozedwa ndi wapampando wake, a Walter Nyamilandu Manda, yafika ku Zomba Air base kuti ikamve zambiri zokhuza ndegeyi ndi momwe amagwilira ntchito.

Zidutswa za ndegeyi anadzisamusira ku Zomba pa 18 September 2024.

Olemekezeka Bambo Dyton Milanzi, omwe akuyimira UTM pa chisankho cha pa 30 June 2026 ku Machinga Mikoko Constituency, ak...
21/05/2026

Olemekezeka Bambo Dyton Milanzi, omwe akuyimira UTM pa chisankho cha pa 30 June 2026 ku Machinga Mikoko Constituency, akubwera ndi cholinga chimodzi, kubweretsa chitukuko chenicheni kwa anthu a ku Mikoko. Akufuna kukonza misewu, maphunziro, chipatala, kuthandiza achinyamata komanso kulimbikitsa moyo wa anthu.

Kuvotera Hon. Dyton Milanzi ndiye kuvotera chitukuko ndi tsogolo labwino la anthu a ku Machinga Mikoko Constituency.
*"Utm Tsogolo Lathu.”*

*AMENE SAWONA MALAWI WOSINTHIKA MWA AKABAMBE, AMENEYO NDI M'DANI WADZIKOLI*Munawona nokha mmene ulamuliro wa *boma la MC...
21/05/2026

*AMENE SAWONA MALAWI WOSINTHIKA MWA AKABAMBE, AMENEYO NDI M'DANI WADZIKOLI*

Munawona nokha mmene ulamuliro wa *boma la MCP unachitira*. Amalawi ambiri tinavutika zaka 5 zimene zija.

Panopa aliyense akuwonanso yekha mmene *Boma la DPP likuchitira zinthu zake*. Daily katundu angokwela mtengo ngati dzikoli lilibe olipanga control. Zinthu zofunikira zikusowa m'dziko muno ndipo moyo ukuwawa kwambiri. *FOREX and FUEL* kulibe ndipo ma transport akwela kwambiri kuphatikizapo katundu ofunikira. *Inu a DPP economy si kutema mbamu ayi*

*_Zomsezi nchifukwa choti maboma awiri onsewa la MCP ndi DPP kulibeko akadaulo azachuma ngati_ DR. DALITSO KABAMBE ACHIPANI CHA UTM _amene angasinthe zinthu._*

*AMALAWI 2030 tidzavotere AKABAMBE* amene Ali ndi kuthekera konse kokomzaso CHUMA CHADZIKOLI

*DK2030* nde tsogolo lathu Lowala komanso moyo wokomera aliyense muzonse.

* Project*

Address

Zomba
Zomba
265

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when UTM Youth Achievers 2030 Project posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share