10/05/2026
Youth Nyamula Chikwama! Nthawi Yophula YIF Yakwana!
Kodi mumapanga business? Kapena mumafuna mutapanga business koma mumasowa mpamba?
Kodi mumafuna mutapindula nawo ndi thumba la Youth Innovation Fund?
Nkutheka ena simukudziwa za thumbali..
National Youth Council yakonza mikumano yomwe ikufotokoza za Youth Innovation Fund (YIF) komanso zomwe mukuyenera kuchita kuti muthe kuyiphula ndi thumba limeneli.
Mikumano imeneyi ikuchitika maboma onse mdziko muno ndipo akutambasula mwatsatanetsatane ndondomeko zonse za mmene mungapezere mwayi wa thumba limeneli.
Kwathu kuno nkumano umenewu uchitika motere:
*Malo: Zomba Stadium Hall*
*Nthawi: 1 Koloko masana*
*Tsiku: lolemba pa 11 May 2026*
Mkumanowu uli open kwa wachinyamata wina aliyense kuyambira at youth club or network level, youth organisation ngakhalenso ma individuals.
*Note that there will be no provision of refreshments and transport reimbursement*