02/06/2026
PEMPHERO
mau akuti pemphero safikira penipeni pa tanthauzo lake chifukwa pemphero silitanthauza kupempha kokha koma limatanthauza kupereka nkhawa,mathokozo,kapena uthenga uliwonse kwa Mulungu.
kawirikawiri tikapemphera timakhulupilira kuti Tayankhidwa koma nthawi Zina timakhala kuti sitinayankhidwe,penaso pemphero silinafike.
ena ochepa mwa ma verse amene akukamba za pemphero
1 thessalonians 5:16-18,Mathews 21:22, Philippians 4:6
kodi pemphero ndi la mphamvu bwanji?? ndi paja pamabwera maumboni paja...komaso ndipaja timalowa mu bible kukawona anthu amene adapemphera ambiri mbiri
koma fuso lofunikira kwambiri ndi lakuti kodi KUPEMPHERA kuli ndi nthawi
zimenezi zingathe kuyamba kutipatsanso chithunzithunzi kuti kodi ngati kulibe nthawi nanga kuliso ndi kakhalidwe kake??
okondedwa pa 1 thessalonians 5:17 akunena kuti tizipemphera kosalekeza kusonyeza kuti KUPEMPHERA si mu church Mokha nthawi zonse tikuyenera kukhala tapemphera.
anzathu a chi slam amayenera KUPEMPHERA 50 times a day koma chifukwa chofuna kupereka mpata ku zintchito adachepetsa amapemphera 5 times a day
okondedwa satana amakhala akuyesera every second kuti munthu akhale ochimwa ndithu opanda pemphero palibe chomwe chingayende
pemphero limateteza,pemphero limasintha nyengo,pemphero limachiza nthenda pemphero limafewetsa mitima ya Adani ndipo pemphero limasokoneza ma plan a kumidima.
kodi pemphero likuyenera kuchoka pakamwa pokha??
yankho ndi ayi ,pemphero likuyenera kuchokera mumtima
kusiyana kwa Mulungu ndi mabwana athu a ku office ndikwakuti mabwana athu a mzintchito amafuna amve mau kapena tiwalembere kalata koma Mulungu wathu amawerenga maganizo athu
pamene taganiza zofuna kumchitira wina zabwino Mulungu amakhala wadziwa kale ndipo pamene tikumupempha mu malingaliro athu Mulungu amakhala akumva.
mwapempherako Inu mu minbus pamene driver akuthamangitsa kwambiri.
Mumati Ambuye chonde tithandizeni kuti galimotoyi isachite ngozi
Hannah akuti samkatulutsa mau pakamwa pake pamkangogwedera ndipo Eli adafika pomuganizira kuti waledzera
koma mu mtima mwa Hannah mudali mapemphero 1 Sam 1:26
CONCLUSION
1.kupemphera ndi nthawi Ina iliyonse
2.Mulungu amamva pemphero ngakhale osatulutsa Mau
3.kupemphera si kupempha zosowa kokha komaso kuyamika,ngakhaleso kupembedza
4.mu pemphero muli mphamvu