31/08/2026
Monga ma peer educators, ntchito yawo siimangokhala yogawa uthenga okha basi. Iwowatu, ntchito yawo imakhudza kwambiri pomvetsera mwachidwi, kuyankha mafunso omwe achinyamata amakhala akufunsa, kulongosola momveka bwino nkhani zina zabodza zomwe achinyamata amazikhulupilira komanso kulimbikitsa anthu m'madera mwawo kuti adzipita kuchipatala kukalandira thandizo loyenerera pomwe pafunikira kutero.
Kudzera mumkukambilana kumeneku kwa tsiku ndi tsiku, ma peer educators-wa akuthandizira kuti nkhani zokhudza ubereki wabwino ndi kugonana (SRH) zidzikambidwa poyera komanso momasuka ndiponso kuti njira zamakono zakulera zikupezeka ku madera awo.
Ku bungwe la ECOSID, timakhulupilira kuti anthu a kudera akakhala patsogolo pobwera ndi maganizo kapena njira zomwe zingawapindulire, njira zi zimakhala zokhazikika ndipo zimabweretsa kusintha kwakukulu.