12/06/2026
Tilitonse Foundation Comic Relief UK in Malawi
Adindo kwa mfumu Mabuka m'boma la Mulanje alimbikitsidwa kupitiriza kuzindikiritsa anthu, makamaka achinyamata, njira zochita akachitiridwa nkhanza kuti athandizidwe.
Mkulu woyang'anira ntchito za bungwe la Umunthu Plus m'bomali, a Samson Bwanali, wanena izi pa nkumano wa adindo wowunikira m'mene ntchito yothana ndi nkhanza pakati pa achinyamata ndi aulumali ikuyendera.
Ntchitoyi ndi ya pulojekiti yolimbikitsa ufulu yomwe ikuchitika ndi thandizo la ndalama kuchoka ku Tilitonse Foundation mogwirizana ndi Comic Relief komanso UK International Development.
Iwo anati: "Ndife okondwa kuti anthu tsopano akuzindikira za maufulu awo ndipo nkhanza zikuchepa. Izi zipitirire m'midzimu kuti achinyamata ndi onse olakwiridwa azidziwa zochita. Kulumikizana komwe kulipo pakati pa nthambi za boma ndi adindo ku mudzi kupitirirenso chifukwa olakwiridwa akuthandizidwa ndipo malamulo akugwira ntchito."
Wapampando wa komiti yothetsa nkhanza m'derali, a Margret Sakala, adalonjeza kupitiriza kutumikira modzipereka kuti nkhanza zikhale mbiri yakale komanso tsogolo la achinyamata m'deralo likhale lowala.
Wothandizira zoona zachisamaliro cha anthu m'bomali, a Paul Cheka, adayamikira bungweli pothandiza boma kupangitsa makolo ndi adindo kulemekeza maufulu ndi kuchepetsa nkhanza.
(Wolemba: Temwa Mhone-Correspondent)