09/05/2026
Apolisi m'boma la Mangochi amanga abambo atatu ndi mai mmodzi powaganizira kuti apezeka ndi matumba a makala 108 popanda kalata zowavomereza.
Ofalitsankhani za polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, ati oganiziridwawo ndi a Hawa Kambwiri, Austin Sharifu, Harry Haj, komanso a Shaibu Jonas.
“Anthuwa agwidwa usiku wapa 8 May, 2026 ku Bolera munsewu opita ku Chilipa,” a Daudi anatero.
Anthuwa akaonekera kubwalo lamilandu kukayankha mlandu opezeka ndi makala popanda chilorezo.
Wolemba: Davie Umar