17/03/2026
#
Pamene kuponya voti atseka nthawi ya 4 koloko madzulo ano pa malo ovotera a Malukula Polling Centre ntchito yowerengera mavoti yatha pomwe anthu akuyembekezera mwachidwi kumva zotsatira.
Centre yi yomwe ili ndi ma Polling Station awiri anthu omwe analembetsa kuti adzavota analipo okwana 1913 ndipo omwe avota alipo 806.
Zotsatira zosatsimikizika kuchokera ku Malukula Polling Station 1 zikusonyeza kuti a Aisha Chikoloni a independent apeza mavoti 4, a Lackson Mustafa Jagaji a independent apeza mavoti 2, a Arthur M'dala Kunje a DPP apeza mavoti 174, a Ruth Makwinja a UDF apeza mavoti 94, a James Royidi a Independent apeza mavoti 113 ndipo a Lackson Simba a independent apeza mavoti 26.
Pomwe kuchokera ku Malukula Polling Station 2 zotsatira zosatsimikizika zikusonyeza kuti a Aisha Chikoloni a independent apeza mavoti 9, a Lackson Mustafa Jagaji a independent apeza mavoti 1, a Arthur M'dala Kunje a DPP apeza mavoti 151, a Ruth Makwinja a UDF apeza mavoti 89, a James Royidi a Independent apeza mavoti 115 ndipo a Lackson Simba a independent apeza mavoti 21.
Mavoti owonongeka kuchokera ku Malukula Polling Station 1 analipo asanu (5) pomwe ku Malukula Polling Station 2 voti yowonongeka inalipo imodzi (1) ndipo zotsatira zotsimikizika zikuyembekezeka kulengezedwa ndi bungwe loyendetsa zisankho la MEC likaunikira zonse kuphatikizapo mavoti owonongeka.
(Olemba: Michael Kabuwe - Mangochi)