09/08/2026
BILAL TRUST GIRLS ISLAMIC INSTITUTE
Interview Schedule August 2026
Bungwe la Bilal Trust likudziwitsa makolo ndi asilamu onse kuti linatsekula sukulu yophunzitsira atsikana maphunziro a Muallimah (aphunzitsi a madrassah achikazi) ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre ndipo kuti yakhonza mayeso olowera pa sukuluyi omwe achitikire mmalo awa motere:
LIWONDE MAIN MASJID
MACHINGA
TUESDAY
18 August 2026
01:00 pm
KALONGA MASJID
MANGOCHI
WEDNESDAY
19 August 2026
09:00 am
CHIWINA MASJID (NAMWERA)
MANGOCHI
WEDNESDAY
19 August 2026
12:00 pm
SALIMA MAIN MASJID
SALIMA
FRIDAY
21 August 2026
01:00 pm
TABA MASJID
NKHOTAKOTA
SATURDAY
22 August 2026
09:00 am
LINTHIPE 1
DEDZA
MONDAY
24 August 2026
02:00 pm
HAJRA MASJID (BANGWE)
BLANTYRE
MONDAY
31 August 2026
09:00 am
Ofuna kulemba nawo mayesowa azafunika kukhala:
-Msikana wa zaka zosachepera 20.
-Akhale oti walolezedwa ndi makolo kapena mwamuna wake kugonera ku sukulu kwa MZAKA ZIWIRI za maphunzirowa.
-Akhale kuti amawerenga Qur’ani pena paliponse.
-Akhale okutha kulemba Chiarabu.
ZOFUNIKA KUTENGA
-Cholembera
-Certificate ya MSCE kapena JCE kapena umboni oti anafika form 3 kapena form 4.
-Chiphaso cha umnzika
DZIWANI
-Amene sadzabweretsa chiphaso cha umnzika sadzaloledwa kulemba nawo mayesowa.
-Sukuluyi ndi yaulere, yogonera konko komanso maphunzirowa ndi a MZAKA ZIWIRI.
Mukafuna kumva zambiri imbani foni pa manambala awa: 0999469240 kapena 0888833666 ndipo mudzalankhula ndi Sheikh Abdul Rashid Juma.