25/03/2026
Uwu udali mkumano wa Achinyamata ochokera mmidzi yosiyanasiyana kwa T.A Ngwelero, Cholinga cha mkumanowu chidali kufuna kuphunzitsa Achinyamata za ndondomeko za ngongole ya Achinyamata yomwe boma lidaika kuti Achinyamata azibwereka pofuna kutukulira ma business awo, zinali zopatsa chidwi kuona a Fransis Mwitha omwe ndi mmodzi mwa alangizi odziwika bwino kwa T.A Ngwelero akufotokozera Achinyamata onse ndondomeko zonse zofunikira pa ngongole ya A
chinyamata...
Pomaliza wapampando wa Achinyamata a Amosi Maluwa analimbikitsa Achinyamata onse ayenera kukhala mmagulu Achinyamata ndi cholinga choti azilimbikitsana pa nkhani zosiyanasiyana zokhudza Achinyamata, monga zaulimi, maphunziro, umoyo ndi maluso osiyanasiyana.