08/04/2026
Uthenga Wapadera!
Ngati ntchito imodzi ya Legends yogwira ntchito zachifundo komanso kuthandiza amene ali ovutika ndi osowa, amnzathu owona zachisamaliro anapeza mayi Fatima Binali amene ali ndi ulumali.
Legends inasinkhasinkha thandizo loti tiwatukule amayi Binali kuti akhale odzidalira pa chuma ndipo inaganiza zowathandiza kuti azipanga business ya Mpamba komanso Airtel money.
Kufikira pano, Legends yakwanilitsa zinthu izi:
1. Kupeza kiosk ya TNM yomwe inakaikidwa pakhomo la mayiwa.
2. Kuwaka kapena kuti kuika cement kuti kiosk ikhale yolimba
3. Kuikirila Loko kuti muzikhomedwa komanso
Pakali pano, pakufunika kuti tiwathandize ndi phone (ka mose) yoti azipangira business yandalama zosapitilira MK50,000 komanso mpamba woyambira omwe ndi MK150,000 ( Airtel money.
Tithokoze ma Legends onse polimbikitsa umodzi komanso ntchito za chifundo. Tiyeni tidzakhale limodzi tonse pa mwambo wokapereka Kiosk imeneyi zonse zikakonzedwa.