31/05/2026
π²πΌ ONJEZANI KENANI ATSUTSIDWA KU FUNDO YAKE YOKHALA KUMBALI YA MEC PODELERA BOMA
Kusanthula kwa Symon Mandawala yemwe ali ku United States of America wabweletsa umboni wochuluka wosonyeza kuti Malawi Electoral Commission ikhoza kusamutsidwa ndi boma kupita kumalo ena aliwonse ku Malawi.
Umboni woyamba wochokera ku United States of America. Trump adapambana milandu yonse yomwe inkafuna kuti mabungwe ngati Trade Commission ndi Labor Relations Commission akhale odziimira pa boma. Khoti lalikulu kwambiri ku United States of America linanena momveka bwino kuti ngakhale bungwe ligwire ntchito mwa ufulu wake, silingathe kudzidula pa ulamuliro wa boma. Milandu imeneyi inagwiranso mabungwe akunja ngati USAID.
Umboni wachiwiri ndi wa m'lamulo la Malawi. Gawo la m'lamulo limapatsa Malawi Electoral Commission mphamvu zochita ntchito za zisankho popanda kulamulidwa ndi boma kapena pulezidenti. Koma gawo lomweli limaperekanso kuti ndalama zonse za bungwe zizichokera ku bajeti ya boma. Izi zikutanthauza kuti boma lili ndi dzanja pa moyo wa bungwe kudzera mu ndalama.
Umboni wachitatu wochokera ku mayiko ena. Ku South Africa Independent Electoral Commission imagwira ntchito mwa ufulu wake koma imadalira ndalama za boma la South Africa. Ku Kenya ndi Uganda nkomweko. Mayiko ambiri ku Africa mabungwe a zisankho amadalira ndalama za boma. Izi zikusonyeza kuti ufulu wa ntchito ndi wosiyana ndi ufulu wazachuma.
Umboni wachinayi ndi wakuti ngati Nyumba ya Malamulo ingapange lamulo latsopano lochotsa boma pa udindo wopereka ndalama ku Malawi Electoral Commission, pamenepo bungwe lidzakhala lodziimira kwathunthu. Koma mpaka pano lamulo loterolo palibe.
Malingana ndi kusathura, Mandawala wamaliza kunena kuti ntchito ya Malawi Electoral Commission ndi yodziimira. Koma pazachuma silodziimira pa boma. Chifukwa chake boma likhoza kuisamutsa kumalo kulikonse mkati mwa Malawi osasintha ntchito zake za m'lamulo.
MUDZI WATHU NEWS ONLINE π° | NKHANI ZENIZENI, ZODALIRIKA .