26/08/2026
Episikopi wothandizira mu Arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Vincent Mwakhwawa walangiza akhrisitu omwe alandira sakramenti la Ulimbitso ku parishi ya St. Patrick's Area 18 kuti akuyenera kukhazikika m'moyo wokonda mapemphero komanso kudziletsa ku zochitika zomwe zingasokoneze chikhristu chawo.
Ambuye Mwakhwawa ati kulandira sakramenti la Ulimbitso si mathero a ulendo mu utumiki kwa achinyamata koma chiyambi cha kusinkhasinkha mozama zokhudza mayitanidwe osiyanasiyana.
Iwo adandaulaso kuti maparishi a m'matawuni sakhala ndi chidwi cholimbikitsa achinyamata kulowa unsembe kapena usisteri zomwe zakhala zikuchepetsa chiwerengero cha atumiki mu mpingo wa Katolika choncho apempha makolo kuti adzipereka mpata kwa ana awo kusankha mautumiki osiyanasiyana ndi cholinga chopititsa mpingo patsogolo.
Achinyamata 82 ndi omwe alandira sakramenti la Ulimbitso ku parishi ya St. Patrick's Area 18 mu Arkidayosizi ya Lilongwe.