27/04/2026
๐ ๐๐ง๐ฆ ๐ถ๐ธ๐ต๐ฎ๐๐ถ๐ธ๐ถ๐๐๐ฎ ๐ป๐ฑ๐ผ๐ป๐ฑ๐ผ๐บ๐ฒ๐ธ๐ผ ๐๐ฎ๐๐๐ผ๐ฝ๐ฎ๐ป๐ผ ๐๐ผ๐ด๐ฎ๐๐ถ๐ฟ๐ฎ ๐บ๐ฎ๐ด๐ฎ๐๐ถ ๐ธ๐ ๐ ๐ฎ๐ป๐ด๐ผ๐ฐ๐ต๐ถ
๐๐จ๐ฅ๐๐ฆ๐๐: ๐๐ญ๐จ๐ฅ๐๐ง๐ค๐ก๐๐ง๐ข ๐ฐ๐๐ญ๐ก๐ฎ
Anthu ofunikira thandizo la magazi m'boma la Mangochi tsopano adzilandira thandizoli mosavuta potsatira ndondomeko yatsopano ya Mangochi Blood Distribution Satellite yomwe bungwe lotolera magazi la Malawi Blood Transfusion Service-MBTS, lakhazikitsa.
Poyamba, zipatala za Mangochi, Mulibwanji, St Martins, Koche komanso Monkeybay zakhala zikukatenga magazi ku ofesi ya bungweli ku Balaka, zomwe zimachititsa kuti odwala ena alephere kufikiridwa ndi thandizoli mwachangu.
Izi zimaika miyoyo ya odwala pa chiopsezo kamba koti pena zipatalazi, zimalephera kukatenga magazi ku Balaka mu nthawi yabwino chifukwa chakutalika kwa ntunda.
Koma malinga ndi mkulu wa bungwe la MBTS mchigawo cha ku m'mawa, mayi Edith Chimphamba, bungweli tsopano lidzipititsa lokha magazi pa chipatala cha Mangochi lachisanu lirilonse.
"Tawona kuti ndikofunikira kwambiri kuti ife a MBTS tiyandikire anthu a m'boma lino la Mangochi. Imafikapo nthawi yoti kuno kukufunika magazi mwachangu koma pena kumakhala kovuta kuti achipatala akatenge magazi ku Balaka. Chilinganizo chatsopanochi chithandizira kupulumutsa miyoyo yomwe imatha kukhala pachiopsezo kamba kakusowa kwa magazi," anatero a Chimphamba.
M'mau ake, mkulu woyang'anira malo oyezera zinthu ndikusungira magazi pachipatala cha Mangochi, a Mathias Tembo, anati chilinganizo chatsopanochi chipeputsa kwambiri chipatalachi pankhani yogula mafuta okatengera magazi ku Balaka.
"Ife anthu ogwira ntchito ku chipatala komanso nzika za kuno ku Mangochi ndife okondwa kamba ka chilinganizo chatsopano chomwe a MBTS atikonzera. Ndalama zomwe zimatayika pokatengera magazi ku Balaka tsopano zidzitithandiza pogwirira ntchito zina pa chipatala chino," anatero a Tembo.
Lachisanu pa 24 April 2026, kwa nthawi yoyamba bungwe la MBTS linapititsa lokha magazi ku chipatala cha Mangochi omwe agawidwe ku zipatala zisanu zomwe ziri ndikuthekera kosunga ndi kupereka magazi kwa odwala m'bomali.
Boma la Mangochi limalandira theka la magazi omwe ofesi ya MBTS mchigawo cha ku m'mawa imatolera m'ma boma a Mangochi, Machinga, Balaka, Ntcheu ndi dera la ku m'mawa kwa boma la Dedza.