13/04/2025
Nthawi inayake tinazabwera ndi nkhani yokoma kwambiri ya Mock Wedding mmudzi mwathu mwa Chemboma, cholinga chinali chothandizira bridge yathu ya ku Manda. Mock wedding inatheka ndithu ndipo anthu ammudzi anayipasa moto kwambiri. Komatu sitidathe kufikira target yathu kuti mpaka kuyamba ntchito yomanga bridge. Koma poti CHEYO imakhulupilira kuti chilichonse nchotheka, ndi msokhasokha wathu tayambapo ndithu kumanga bridge yathu ya kumanda.
Mwina m***a kufunitsisa kukhala nawo modzi ochita zithu zabwinozi please tiyakhuleni tiyendere limodzi.
Muzithuzimu mukuonetsa bridge yakale ndi bridge yasopano yomwe yayamba kumangidwa.
Mu umodzi muli mphamvu..
Chemboma Youth Organization-CHEYO