13/03/2026
NDI 150,000 YOKHA.
Before you think of going to South Africa, read this or kaya muli kale komweko, please read.
Zimangovuta guys kt ambiri amaona ngati kupita ku South Africa kuthandiza kuchepesa mavuto awo koma zoona zenizeni ndi zoti 90% ya anthu amene anapita kumene kuja akuvutika kuposanso kumangokhala kwathu konkuno.
Kodi tray yama dzila amagula ndalama zingati?
Tiyelekeze kt ndi 15,000 like 500 each.
Koma madzila a boil aja ma guys amagulisa ma 700 mma pub umu timaona ife.
That means kupanga boil madzila pa Crete profit ndi 6000 and ngati mwagulisa ma Crete awiri pa siku ndie kt pa siku mwapanga Profit ya 12,000.
MUSANAPITE KU SOUTH TAYESANI KAE IZI BWA;
150,000 Budget yanu.
90,000 gulani ma Crete 6 amadzira.
Gulani ma bucket owonekera mkati atatu.
Gulani Saboola ndi mchere plus ma bottles ake.
Pitani ku mudzi mukatenge anyamata osowa zochita muwalembe ntchito yogulisa madzila a boiled aja.
Chakudya chanu komanso malo ogona anu Madzulo okha cz masana azidya koyenda (azichosa 500)
Aliyense target ma tray awiri ndipo amene azikwanilisa target yake daily Salary yake izikwera ndi 10,000 (u can use anything to Motivate them work hard).
LET'S MAKE CALCULATIONS NOW:
Listen guys:
Business is about calculations.
If you can not calculate, you can't make business cz it is this calculations that gives you energy to continue or stop.
GO.
Mwana aliyense per day akubwelesa 11500 Profit making 34,500 everyday.
Pa mwezi anawa akukupangilani gross profit ya 1,035,000.
Remember ndalama imeneyi capital yake ndi 150,000 yokha basi.
Kodi pamenepapa mukachosapo malipiro awo plus chakudya chomwe akudya ndalama yomwe ikusala siyokwanila kuti mungokhala ku Malawi konkuno?
Guys zimandikhuza ndikakumana ndi a Malawi a nzanga kunjako mmene akuvutikila after spending ndalama Zambiri mbiri on Transport plus passport kuti akapezeke kumeneko.
At one point mpaka I sold top yanga mu bus momwemo ndalamazo kusiila nyamata wina amene a police ya Mozambique anamusisa komanso kumumanga after akt ma transporter atamudyela ndalama zake zonse.
At one time I sold my phone in Maputo to help a certain guy amene anathawa ndende via Maputo kuti apeze Transport yofikila ku mw kuno.
I have seen many Malawians suffering in the streets of Jubek kulakalaka atangopeza mayendedwe oti apezeke kuno kwathu.
Just pa TETE pomwepa ziko la Mozambique, everyday pakufika a Malawi osowa thandizo akugona pansi peni peni.
GUYS, UMPHAWI SIKUSOWA KWA NDALAMA KAPENA MATERIALS AI. UMPHAWI NDI KUSOWA KWA MZERU KAPENA KUTI UPANGILI.