25/09/2026
NDINU ALUSO?
Kodi mumadziwa kuti luso lanu lingabweretse kusintha mdera lanu?
LICEDO ikukupatsani mwayi wowonetsa luso lanu pa Skills Competition!
Pangani kanema wa mphindi zitatu (3 minutes) kapena kuchepera wokhudza imodzi mwa mitu iyi:
1. Mmela ndimpoyamba (Early Childhood Development)
2. Maphunziro (Education)
3. Kutukula Achinyamata ndi Azimayi (Youth and Women Empowerment)
MMENE MUNGATENGERE NAWO MBALI
1. Like page ya LICEDO.
2. Jambulani kanema wanu pogwiritsa ntchito foni kapena camera.
3. Tumizani kanema wanu wopanda watermark, nyimbo kapena zinthu zina zowonjezera ku WhatsApp:
0880 699 026
Simukufunika zipangizo zodula. Foni yanu yokha ndiyokwanira. Chofunika ndi luso lanu, umwini komanso uthenga wanu.
WOPAMBANA ADZASANKHIDWA POTENGERA:
Luso
Umwini
Uthenga
Makanema 6 adzasankhidwa ndi komiti ndikuyikidwa pa page ya LICEDO. Anthu adzavota kudzera mu ma likes, ndipo mavoti awo adzathandiza kusankha wopambana.
Musabise luso lanu. Lisonyezeni. Pangani uthenga. Bweretsani kusintha.
TUKULANI MALUSO ANU NDI LICEDO!