21/04/2026
Mkulu wa bungwe la Youth Association for Conservation of Nature and Environment (Yascon) Mwai Mtayamanja wati bungwe lawo lakwanitsa kubzala mbande za mitengo zopitirura 3 000 m'nyengo yobzala mitengo ya 2025/26 yomwe yangotha kumene.
Malingana ndi Mtayamanja, mlingowu ndi wochepa poyerekeza ndi momwe amayembekezera komabe ati kupitiriza mgwirizano wawo ndi achinyamata m'dziko muno kutha kuthandiza kupititsa patsogolo ntchito yosamalira ndi kubwezeretsa chilengedwe.
Iwo atinso mavuto a ng'amba ndi kusefukira kwa madzi zomwe zidakhudza madera ena zidapsinja mmene bungweli limayenera kugwirira ntchito yake m'nyengoyi.
Komabe, a Mtayamanja ati apitiriza kugwira ntchito ndi magulu osiyasiyana poonetsetsa kuti achinyamata akuikidwa patsogolo pa ntchito yoteteza, kubwenzeretsa komanso kusamalira chilengedwe.
Bungwe la Yascon lomwe limalimbikitsa achinyamata kutenga nawo gawo poteteza, kubwezeretsa ndi kusamalira za chilengedwe likugwira ntchitoyi m'maiko angapo kuphatikizapo Malawi, Kenya ndi Uganda.
(Wolemba Chrispine Msiska-Correspondent)