Malawi Coalition for Kabaza Stakeholders and Associations. Macokasa

  • Home
  • Malawi
  • Lilongwe
  • Malawi Coalition for Kabaza Stakeholders and Associations. Macokasa

Malawi Coalition for Kabaza Stakeholders and Associations. Macokasa MACOKASA is dedicated to building a safer, organized, and empowered kabaza industry in Malawi.

Through partnership and advocacy, we prioritize rider welfare, regulatory compliance, and sustainable growth.
‎
‎Members: ROSAF | KATAMAS | K**A.

16/06/2026

‎Mtsogoleri wa bungwe la MACOKASA, Moses Michael Mwalabu, anali mdziko la Rwanda kuyambila pa 30 May mpaka pa 5 June motsogozedwa ndi unduna oona za maboma ang'ono ang'ono ndi chitukukuko cha m'madera, komwe anaphunzira zambili zokhudza Kabaza.
‎
‎Kutsatira izi, bungwe la MACOKASA laika ndondomeko zosiyanasiyana, pofuna kuphunzitsa akabaza momwe dziko la Rwanda limachitira, ndi kukwanilitsa ndondomeko zina mdziko lino.
‎
‎Kotero, bungweli likhala likukhazikitsa magulu a kabaza a m'mizinda, pofuna kukwanilitsa ndondomekozi mosavuta.
‎
‎Kanema ali m'musiyi akuonetsa zambili zokhudza ulendowu, komanso mmene akabaza ku Rwanda akugwilira ntchito zawo za pansewu.
‎
‎

02/06/2026

‎Dziko la Malawi liyembekezere kusinthika kwakukulu kamba ka ulendo waku Rwanda omwe bungwe la MACOKASA layenda motsogozedwa ndi unduna oona za maboma ang'ono ang'ono ndi chitukukuko cha mmadera, ndi thandizo lochokela ku bungwe loyang'anira za chitukuko padziko lonse la UNDP, ndi banki ya FDH.
‎
‎Kudzikoli maguluwa analandilidwa ndi bungwe lolimbikitsa mgwirizano la boma la Rwanda lotchedwa Rwanda Cooperation, lomwe linaonetsa chitukuko cha misewu ndi masomphenya adziko la Rwanda.
‎
‎Maguluwa aphunziranso mmene apolisi ndi akabaza amagwilira ntchito zawo zapamsewu, komanso kutsatira malamulo ndi zina monga kulembetsa njinga, kulembetsa umembala ku bungwe la akabaza, kuimika njinga malo oyenelera, kuvala zipewa za njinga ndi kunyamula anthu ndi katundu wa mulingo oyenelera.
‎
‎Ulendowu unayambika pa 30 May, ndipo ukhala ukupitilira mpaka pa 5 June, pomwe bungwe la MACOKASA, nthambi za boma ndi magulu ena, akhale akupitilira kuphunzira za chitukuko ndi masomphenya a dziko la Rwanda.
‎
‎

‎Unduna oona za maboma ang'ono ang'ono ndi chitukuko cha m'madera, waganizira akabaza potenga mtsogoleri wawo Moses Mich...
24/05/2026

‎Unduna oona za maboma ang'ono ang'ono ndi chitukuko cha m'madera, waganizira akabaza potenga mtsogoleri wawo Moses Michael Mwalabu, paulendo opita ku Kigali Rwanda omwe ukhalepo pa 30 May mpaka pa 5 June, kuti akaphunzire mmene maiko ena akuchitira zinthu.
‎
‎Cholinga chaulendowu ndikufuna kupititsa patsogolo maubale adziko lino ndi maiko ena, komanso kuonetsetsa kuti akabaza akugwira ntchito zapamsewu mwaukadaulo pophunzira kachitidwe ka maiko ena.
‎
‎Kuonjezera apo, ulendowu uthandiziranso kupititsa patsogolo chitetezo chapansewu, komanso kukhala ndi mizinda yosamalika mdziko lino.
‎
‎Rwanda ndi dziko lodziwika bwino pankhani ya ukhondo ndi ndondomeko zina zachuma mu Africa, ndipo aka kakhala koyamba kuti akabaza mdziko lino akaphunzire kuchokela kudzikoli.
‎
‎

27/02/2026

‎Boma tsopano lamva madandaulo a aKabaza otsogozedwa ndi bungwe la MACOKASA, pomwe lapeleka mwayi wa miyezi 6 kuyambila mwezi wa April, kuti aKabaza akhale atalembetsa njinga zawo.
‎
‎Izi zikutanthauza kuti njinga zonse zosalembetsa ziyamba kugwidwa mu mwezi wa October, ndi kulandila chilango monga mwa lamulo.
‎
‎Komabe, bungwe la MACOKASA, apolisi ndi magulu ena, apitiliza kugwila njinga za anthu osavala zipewa zodzitetezera kungozi, onyamula katundu mopyola muyezo ndi ena onse ophwanya malamulo a pamsewu, pofuna kuchepetsa ngozi ndi imfa zodza kamba ka mchitidwewu.
‎
‎Tiyeni tigwilitse ntchito bwino mwayi omwe boma lapeleka, kutsatira malamulo ndi njira zonse zodzitetezera kungozi ndi mavuto ena a pamsewu.
‎
‎

‎KuZombanso taziyambitsa! 🔥🙌🙌🙌‎‎Bungwe la MACOKASA, mogwilizana ndi khonsolo ya mzinda wa Zomba, apolisi, a Traffic, a P...
18/02/2026

‎KuZombanso taziyambitsa! 🔥🙌🙌🙌
‎
‎Bungwe la MACOKASA, mogwilizana ndi khonsolo ya mzinda wa Zomba, apolisi, a Traffic, a Passion Center ndi magulu ena, pa 17 February lakhazikitsa ntchito yolimbikitsa chitetezo cha akabaza ndi kutsatira malamulo apamsewu mumzinda wa Zomba.
‎
‎Ntchitoyi yomwe inatsogoleledwa ndi mfumu ya mzindawu Christopher Jana, inayamba ndi mkumano omwe unachitikila kukhonsolo ya mzindawu, pomwe magulu osiyanasiyana amagawana maganizo pamfundo zopititsila patsogolo chitetezo cha akabaza ndi anthu onse mdziko lino.
‎
‎Mwazina, aJana anaunikila kufunika kopititsa patsogolo ntchito yolimbikitsa kutsatira malamulo apamsewu monga kulembetsa njinga zamoto, ndi ndondomeko zodziteteza kungozi zapamsewu, monga kuvala zipewa ndi kunyamula katundu pa mulingo oyenelera.
‎
‎Kumbali yake, mtsogoleri wa MACOKASA Moses Michael Mwalabu, anagwilizana maganizo ndi aJana, ndi kutsindika kuti ophwanya malamulowa akuyenela kulandila chilango kapena kupeleka chindapusa monga mwa lamulo.
‎
‎Mwezi watha, bungwe la MACOKASA ndi maguluwa linakhazikitsa ntchitozi mumzinda wa Blantyre, pomwe mawa lino likhazikitsenso ku Mangochi, ndi chiyembekezo chofalitsa mmadela ena mdziko lino.
‎
‎

02/02/2026
‎MACOKASA ENGAGES MINISTRY OF HOMELAND SECURITY ON KABAZA SAFETY AND FORMALIZATION‎‎The Malawi Coalition for Kabaza Stak...
19/01/2026

‎MACOKASA ENGAGES MINISTRY OF HOMELAND SECURITY ON KABAZA SAFETY AND FORMALIZATION
‎
‎The Malawi Coalition for Kabaza Stakeholders and Associations (MACOKASA), on 19 January engaged the Ministry of Homeland Security and key stakeholders at Capital Hill in Lilongwe, to strengthen collaboration on Kabaza safety, law compliance, and formalization.
‎
‎The meeting, presided over by Minister of Homeland Security Hon. Peter Mukhitho, brought together officials from the Ministry, the Malawi Police Service, the Directorate of Road Traffic and Safety Services, Lilongwe City Council, Community Policing, the Ministry of Local Government, the Ministry of Finance, and other partners.
‎
‎The Minister acknowledged Kabaza’s contribution to transportation and employment, reaffirming government commitment to coordinated action, compliance with highway codes, proper registration, and stakeholder collaboration to address challenges including road accidents, killings, and theft.
‎
‎He further assured action against individuals illegally controlling Kabaza ranks and extorting money from operators, commonly known as 'migodi', stating that the Ministry will work closely with the Malawi Police Service to address the issue as such practices operate outside the law.
‎
‎MACOKASA Chairperson Mr. Moses Michael Mwalabu highlighted key challenges facing the sector, including road safety, registration and licensing, fair fees, access to loans, and the need to reduce accidents, crime, and migodi activities.
‎
‎Stakeholders agreed on the need for stronger enforcement, formalization of Kabaza operations, training of operators, use of protective equipment such as helmets and reflectors, insurance uptake, and continued collaboration to build a safer and well-regulated Kabaza sector.
‎
‎
Malawi Government
Malawi Police ServiceMinistry of Local Government and Rural Development-Malawi

‎Bungwe la MACOKASA, lakangalika pantchito za chitetezo cha aKabaza, zotsatira malamulo a pamsewu, ndi kufikitsa ntchito...
17/01/2026

‎Bungwe la MACOKASA, lakangalika pantchito za chitetezo cha aKabaza, zotsatira malamulo a pamsewu, ndi kufikitsa ntchitozi kumadela ena mdziko lino.
‎
‎Izi zikudza pomwe bungweli mogwilizana ndi magulu ena okhudzidwa, akhazikitsa ntchito zogwila aKabaza ophwanya malamulo a pamsewu mumzinda wa Blantyre.
‎
‎Pa 13 January, Bungweli linachita mkumano ndi akulu akulu a mzindawu, makhansala, apolisi, otolera misonkho, oona za malamulo a pamsewu, ochita malonda a Kabaza ndi magulu ena ku khonsolo ya mzindawu, kukambilana zolimbikitsa chitetezo cha aKabaza komanso zotsatila malamulo a pamsewu.
‎
‎Zitatha izi, pa 14 January, maguluwa anapita kumsika waukulu wa Limbe komwe anagwila njinga za aKabaza osavala zipewa zanjinga, komanso omwe amanyamula katundu mopyola muyezo.
‎
‎Bungwe la MACOKASA mogwilizana ndi magulu okhudzidwa, likupitilira kuchita zokambilana kuti aKabaza akhale otetezeka, atsatile malamulo a pamsewu, komanso kuti pakhale mitengo yabwino yolembetsela njinga, pofuna kuthetsa ngozi zapamsewu zokhudza aKabaza, kuphedwa ndi kubeledwa njinga zawo.
‎
‎
‎

‎JOINT STAKEHOLDER EFFORTS LAUNCHED TO ADDRESS KABAZA CHALLENGES IN BLANTYRE CITY ‎‎The Malawi Coalition for Kabaza Stak...
17/01/2026

‎JOINT STAKEHOLDER EFFORTS LAUNCHED TO ADDRESS KABAZA CHALLENGES IN BLANTYRE CITY
‎
‎The Malawi Coalition for Kabaza Stakeholders and Associations (MACOKASA) has officially extended its road safety and law compliance activities to Blantyre City, marking a major step in strengthening safety, regulation, and coordination within Kabaza operations in the city.
‎
‎On 13 January, MACOKASA convened a multi-stakeholder engagement meeting at Blantyre City Council, bringing together the City Council, City Councillors, the Directorate of Road Traffic and Safety Services, the Malawi Police Service, the Malawi Revenue Authority, the Road Safety Alert Foundation (ROSAF), Kabaza consultants, owners, operators, and other partners.
‎
‎The engagement, presided over by Blantyre City Deputy Mayor, Councillor Gerald Lipikwe, focused on addressing key Kabaza challenges including road safety, compliance, crime, and regulation, as MACOKASA expands its operational footprint beyond Lilongwe.
‎
‎Stakeholders reaffirmed their commitment to collaboration, with the City Council and Malawi Police Service pledging to strengthen enforcement in high-risk areas prone to Kabaza-related attacks, theft, and road accidents. Emphasis was also placed on public sensitization, improved communication, and coordinated enforcement strategies.
‎
‎As part of the extension, practical joint enforcement actions were conducted in Limbe on 14 January, where stakeholders collectively supervised Kabaza operations, reinforcing compliance with helmet use, load limits, and traffic regulations.
‎
‎The Blantyre engagement follows MACOKASA’s ongoing national efforts to promote safe roads, lawful operations, and improved welfare for Kabaza operators, with similar activities planned for other districts that have signed Memoranda of Understanding with the coalition.
‎
‎MACOKASA remains committed to working with government and partners to build a safer, regulated, and sustainable Kabaza sector across Malawi.
‎
‎
‎

14/01/2026

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Malawi Coalition for Kabaza Stakeholders and Associations. Macokasa posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share