08/06/2026
MINUTES OF THE NDIFE AMODZI GROUP MEETING
• *Date* : 7 June 2026
• *Time* : 4:00 PM
• *Venue* : Kunyumba kwa a Kachere
*Opezekapo: Mamembala Omwe Analipo*
1. Anastanzia Kachere
2. Charity Chipofya
3. Gift Malenga
4. Alinafe Mlotha
5. Chimwemwe Bester
6. Gracious Chipofya
7. Mr. Tsoka
*Zolinga za mu Gulu ndi Thandizo la Ma Membala (Social Welfare)*
•Ma members adakambirana mozama za kukhazikitsa dongosolo la kasamalidwe ka ma members, powona kuti monga gulu logwirizana, ndikofunikira kuthandizana pakachitika zinthu zadzidzidzi monga maliro komanso matenda.
•Zotsatirazi ndi zomwe zagwirizanidwa pokhudza kayendetsedwe ka dongosololi:
•Oyenerera Kuthandizidwa: Thandizoli liziperekedwa kokha kwa mamembala omwe ali active pazochitika za gulu amene azakhale kuti afeledwa ndi achibale omwe ndi makolo, ana a munthu ofeledwa kapena achibale cha pafupi).
Kulembetsa kuti umembala ukhale wovomerezeka, gulu lakhazikitsa ndalama zolembesera u membership fee 1,000 ndi 1,000 yopelekedwa pa mwenzi
*Kapezedwe ka Ndalama:* Ndalama zothandizira mamembala zizitengedwa mwandondomeko m’thumba la ndalama zolembesera komanso zoyendetsera umembala.
*Chipepeso cha Maliro:* Ngati membala yemwe ali m'gulu wakumana ndi zovuta monga maliro, gululi lizipereka ndalama zokwana MK 20,000 zochokera m'thumba la chithandizoli kuti zithandizire pa maliro.
*Thandizo la Matenda/Kugonekedwa Chipatala* : Membala akadwala, gululi lizipatula MK 10,000 yoti yomuthandizila.
_Chonde tikuyenela kuziwa kuti apa ndi poyambila chabe pa gulu ngati kuli kusintha kuli konse gulu lizawuzidwa ndipo izi zapelekedwa kuwonaso mmene ma members omwe tili nawo ngati gulu_
*Komiti ya Chithandizo (Welfare Committee):* Zidagwirizana kuti pakufunika kusankhidwa Mtsogoleri kapena Komiti ya Chithandizo yomwe iziyang'anira komanso kuyendetsa bwino dipatimentiyi.
2. *Kugwirizana ndi Mafumu/Atsogoleri a m'Dera*
Gululi lidakambirana za kulimbitsa ubale ndi atsogoleri a m'derali ndipo lidagwirizana zokayendera atsog
Send a message to learn more