11/12/2025
Dzulo pa 10th December 2025 tamaliza bwino kampeni ya Masiku 16 Otsutsa Nkhanza zapakati pa amayi ndi atsikana . Chaka chino, dziko lonse limakumbukira motsogozedwa ndi mutu ofunikira uwu: 🔥 UNiTE to End Digital Violence against All Women and Girls "Tiyeni Tigwirizane pothetsa Nkhanza Za Pa Intaneti Zokhudza Amayi ndi Atsikana".
Kwa masiku 16 apitawa, CECOYD, kudzera mwa ma peer civic educators ake, yakhala ikulowamo m'madera, kuphunzitsa anthu, ndikulimbikitsa achinyamata komanso mabanja kufunika kuthetsa nkhanza zonse, kuphatikiza nkhanza za pa intaneti zomwe zikukula tsiku ndi tsiku. Kuyambira pa zokambirana za m’madera mpaka ku misonkhano ya achinyamata, cholinga chathu chakhala chimodzi: tsikana komaso mayi aliyense ayenera chitetezo, ulemu, ndi mtendere Ku nkhaza zodzera pa intaneti.
🙏 Tikuthokoza kwambiri anzathu onse ogwira nawo ntchito , atsogoleri a m’madera, magulu a achinyamata, komanso aliyense amene anatenga gawo pa kampeni imeneyi.
Ngakhale kampeni ya masiku 10 yamalizika chaka chino, ntchito yathu siyiyima. Pamodzi, tipitiriza kulimbikira kuti Malawi akhale malo otetezeka kumene amayi ndi atsikana angakule mantha m’malo onse omwe amakhala.