07/03/2025
📢 DZINA MWA ZOMWE WANENA JB PA ZODIAK EXCLUSIVE
1️⃣🏠 "President Chakwera tinakumana pomwe ankandisankha kukhala ambassador wa goodwill wa za Cyclone Freddy. Anatiuza kuti adzatiitana kuti tikakambilane za budget kuti timange nyumba za anthu, koma mpakana lero. Moti ine nyumba zomwe munkaona ndimayendera zamangidwa ndi Joyce Banda Foundation."
2️⃣💰 "Chuma cha dziko lino sichikuyenda, pali mavuto. Chiyambileni, katundu sanakwerepo katatu pa tsiku, 1 dollar mpakana kumagulisidwa 5,000 Malawi Kwacha. Ngati dziko tikufunika kupeza njira zoti tipedzere ndalama zakunja."
3️⃣🌱 "Amene ankakamba za ma Mega Farm ndi Saulos Chilima, a Chakwera ankakamba za High 5. Green Belt ili kuti? ADMARC ili kuti? Chifukwa Green Belt bwenzi ikutithandiza kulima chakudya chokwanira."
4️⃣🚔 "Ukakhala president zambiri sumadzidziwa zikamachitika kunja, chifukwa kunjaku anthu amatakata (kuba/katangale). Nde ukawadziwa umawachotsa ntchito ngati momwe achitira President Chakwera. Ena amafunika kumangidwa kuti azikuopa, so Ukakhala kuti nawe so ndiwe wa katangale, nde amakuophyeza kuti tikuwululani."
5️⃣📉 "Kuti zinthu ziyende m'Malawi muno, tikufunika tithetse kaye katangale, komanso tipeze forex."
6️⃣🌍 "Ubale wathu ndi maiko akunja sikuti unaipa. Nthawi yomwe ndimalowa ine, mpamene ubale sunali bwino. Tonse tikukumbukira kuti dziko la Britain ubale tinathetsa (titha kupempha maiko akunja kuti atithandize kupeza forex)."
7️⃣🏗️ "Ndikudabwa kuti nyumba zomwe ndinamanga ine through Joyce Banda Foundation zikupezeka mu SONA, watiyezeka."