19/08/2026
https://web.facebook.com/share/p/1CxTh616QK/
Ngati njira imodzi yochepetsera kuchuluka kwa akaidi m'ndende za m'dziko muno bungwe la Para legal Advisory Service Institute (Pasi) achititsa maphunziro kwa nzika za m'boma la Mwanza a mmene angathanirane ndi milandu ing'onoing'ono m'madera mwawo.
Mkulu wa bungweli m'boma la Mwanza a Chimwemwe Ndalahoma, ati apeza kuti m'ndende za m'dziko muno mukudzadza ndi milandu yoti ikanathera ku madera, choncho kunali koyenera kupereka maphunzirowa kuti anthu azitha kukambirana ndi kuthera konko.
"Ku ndende zathu kukudzadza ndi milandu yoberana mandalena, nkhuku komanso phava limodzi la nthochi zomwe zitha kuthera m'makomo momwemu pamene anthu akhala pansi ndi kukambirana chifukwa sichilichonse chikufunika ku polisi", aatero a Ndalahoma
Mkulu wa ndende ya Mwanza mayi Mary Mbonekera ati izi zithandiza kuti ndende zizikhala ndi anthu okhawo omwe ali ndi nthawi yaitali zomwe zimaperekanso danga lophunzira luso losiyanasiyana.
"Pano ku ndende si malo olangira koma ophunzirira, kotero pamene mwamutumiza munthu kwa miyezi yochepa chabe palibe chomwe angaphunzire kuti zikamuthandize pamene watuluka kundende," atero a Mbonekera
Mfumu yaikulu Nthache yati maphunzirowa alimbikitsa umodzi kumadera komanso athandiza kuchepetsa ntchito ya mafumu yoweruza milandu ina ing'ono ing'ono.
Mmodzi mwa omwe achita nawo maphunzirowa mayi Yvonne Phineas, ati akagwiritsa ntchito ukadaulo omwe aphunzira pokhazikitsa bata ndi mtendele kudera lawo.
Bungwe la PASI likuchitsa maphunzirowa pansi pa pulojekiti yomwe ikuchitika ndi thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe la European Union (EU) komanso Unicef ndipo ichitika Kwa zaka zinayi.
Wolemba Doreen Chiwalo Correspondent