Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC

Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC, Youth Organization, P/Bag 19, Kasungu.

The aim it's to provide accessible, confidential, and non-judgmental care, focusing on sexual and reproductive health, HIV prevention, mental health support, and youth empowerment

Hello achinyamata a m'boma la Kasungu!Mudayamba mwamvapo mawu akuti, "mbewa yamanyazi idafera kuwuna", kapena kuti "msus...
28/08/2026

Hello achinyamata a m'boma la Kasungu!

Mudayamba mwamvapo mawu akuti, "mbewa yamanyazi idafera kuwuna", kapena kuti "msusu watherere sayika kumpani?"

Indeeee! Musalole kuti tsogolo lanu lifere m'mazira kaamba koti mwatenga pathupi kapena matenda opatsirana pogonana mukadali achichepere m'bomali.

Bwerani kuchipatala chathu chachikulu cha Kasungu, kapena chomwe mwayandikana nachiko m'dera lanu, kuti mukatenge makondomu kapena njira zina zodzitetezera ku vutoli.

& Neonatal health, and GBV awareness campaign in Kasungu Municipality.

NB: Activity performances by Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC.

Ministry Of Health - Malawi Kasungu District Council Malawi Government Family Planning Association of Malawi IM Swedish Development Partner Southern Africa Youth Wave Malawi Kapiri Community Development Organization UNICEF Malawi National Youth Council of Malawi

-Youth Corner
No One Behind

Imfa eeeh, ndiwe dolo! Watitengera mzati wathu, Dalitso Phiri, yemwe timadalira pa nkhani yofalitsa uthenga wa zaumoyo w...
07/08/2026

Imfa eeeh, ndiwe dolo! Watitengera mzati wathu, Dalitso Phiri, yemwe timadalira pa nkhani yofalitsa uthenga wa zaumoyo wa achinyamata ku Kasungu.

Ulendo wako waliza anthu ambiri, moti Ife tinakukonda kuti ukanakhala nafe kwa muyaya, koma lero wawolokera tsidya lina.

Mzimu wako uwuse m'tendere mpaka kufikira pomwe tidzakumaneso muulemelero.

Pomaliza, Ife a Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC, tikuthokoza ofesi ya Zaumoyo m'bomali, Hon. Noel Mkubwi MP, YAM-Malawi, Zotheka, Kasalika YFHS, Red Cross, ndi achinyamata onse amene tinali limodzi kwa Kawiza m'dera la mfumu yayikulu Kaomba, m'bomali.

Ministry Of Health - Malawi Malawi Government Kasungu District Council IM Swedish Development Partner Southern Africa Youth Wave Malawi Kapiri Community Development Organization

-Youth Corner
No One Behind

Mkulu oyang'anira za umoyo wa amayi ndi ana m'boma la Kasungu, a Baziwell Malisen, walimbikitsa anthu m'bomali kuti agwi...
02/08/2026

Mkulu oyang'anira za umoyo wa amayi ndi ana m'boma la Kasungu, a Baziwell Malisen, walimbikitsa anthu m'bomali kuti agwirane manja popitsa patsogolo ntchito zaumoyo mbomali.

A Malisen amayankhula izi kwa Jembe, m'dera la mfumu yayikulu Wimbe m'bomali, pa mwambo ozindikiritsa anthu za thandizo la zaumoyo lomwe likuperekedwa m'deralo monga kuunika amayi omwe ndi oyembekezera, TB, kupereka njira zakulera, komanso thandizo la achinyamata (YFHS), mwazina.

Malinga ndi a Baziwell, izi zili ndi kuthekera kochepetsa mavuto omwe anthu akukumana nawo m'bomali monga kutalika kwa mitunda yomwe ena amayenda usaka thandizo la chipatala kaamba koti kuderako kulibe malo abwino olandilirapo thandizo la chipatala ndi nyumba za ogwira ntchito.

M'mawu ake mfumu Jembe ya m'deralo, yati ndi yodzipereka utukula ntchito zaumoyo m'deralo pamodzi ndi mafumu ena.

Nawo achinyamata a Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC anali nawo pa mwambowu, kupereka msangulutso kudzera m'masewero komanso kuvina mwazina.

Ministry Of Health - Malawi Kasungu District Council Malawi Government Family Planning Association of Malawi IM Swedish Development Partner Southern Africa Girls Empowerment Network Youth Wave Malawi UNICEF Malawi

-Youth Corner
No One Behind

Nthawi zambiri foni ikangofika pa 10%, anthu ambiri timathamanga ukayika patchaji, kuopa kuti ingamiziretu. Nde ikakhala...
29/07/2026

Nthawi zambiri foni ikangofika pa 10%, anthu ambiri timathamanga ukayika patchaji, kuopa kuti ingamiziretu. Nde ikakhala kuti nsima yalimba kale mkandiro, pomwe ukuyika magetsi amadzazima ngati mwana wa aneba wagwetsa "main switch" nsima ikubwata 😀

Funso, mkumati n'chifukwa chiyani achinyamata ambiri a m'boma lino la Kasungu, mumadikira kuti moyo wanu udutse kaye pa 10%, kenako mkumapita kuchipatala ukasaka thandizo, injini yanu italowa kale madzi?

Matenda ambiri samayimba wezulo akamabwera, umawazindikira nthawi itatha kale, khirisimasi ndi nyuwere itadutsa kale, iwe uyesera ukwera kapalasa kumangogwa tcheni ngakhale kuti ndi kumatsitso 😀

Pofuna kupewa izi, Lachisanu likudzali pa 31 July, 2026, tiyeni tikumane pa msika wa Linga, m'manisipalite ya m'boma la Kasungu, pomwe ife a Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC limodzi ndi akatswiri azaumoyo tikhale tikupereka thandizo losiyanasiya kwa achinyamata a m'derali, monga kuyezetsa matenda opatsirana pogonana, makondomu, uphungu komanso upangiri wa momwe angatetezere thanzi komanso tsogolo lawo mwazina.

M'nyamata otsogola sangoyika password pa phone yake yokha, amatetezanso ngakhale tsogolo lake.

Ministry Of Health - Malawi Malawi Government Kasungu District Council Development Network for Youth Empowerment - Deneye IM Swedish Development Partner Southern Africa Family Planning Association of Malawi Futureafricaleadersfoundation

-Youth Corner
No One Behind

Nthawi zambiri, achinyamata ena amafuna thandizo la zaumoyo mavuto akafika pothina kapena poning'ina, monga kutenga mimb...
26/07/2026

Nthawi zambiri, achinyamata ena amafuna thandizo la zaumoyo mavuto akafika pothina kapena poning'ina, monga kutenga mimba akadali achichepere komanso matenda opatsirana pogonana mwazina.

Ngakhale kuti izi zili chomwechi, lero m'madera a kwa Juma, Mumba ndi Kaning'a m'manisipalite ya Kasungu, ambiri apanga chisankho chotenga njira zodzitetezera kumavutowa zomwe tinapititsira m'madera awo.

M'modzi mwa atsogoleri a Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC komanso yemwe ndi YCBCDA, Asam Dafutala, wati ndi okondwa kuona achinyamata ambiri patsikuli akupeza mwayi wa uthenga wa umoyo wawo wangiro komanso kutenga njira zakulera monga makondomu, mapilisi a pangozi mwazina zomwe zingatukule thanzi lawo m'maderawa.

Malinga ndi Dafutala, ntchitoyi ikhala ikupitirira pa 31 mwezi uno ku Linga, komwe ndi kuseli kwa phiri la Ngulayanambe, m'manisipaliteyi, pofuna kuchepetsa mavuto omwe achinyamata akukumana nawo m'bomali.

Ministry Of Health - Malawi Development Network for Youth Empowerment - Deneye Malawi Government Kasungu District Council IM Swedish Development Partner Southern Africa Banja La Mtsogolo Girls on the lead young feminist movement Youth Wave Malawi.

-Youth Corner
No One Behind

Kawirikawiri nthawi ya holide ngati ino, imapereka mpata kwa ophunzira kuti atha kupuma mokwanira, kucheza ndi anzawo, m...
26/07/2026

Kawirikawiri nthawi ya holide ngati ino, imapereka mpata kwa ophunzira kuti atha kupuma mokwanira, kucheza ndi anzawo, makolo ndi achibale ena.

Ngakhale kuti izi zili chomwechi, ndi nthawi yomwe achinyamata ambiri amakumana ndi mavuto monga kutenga pathupi komanso matenda opatsirana pogonana, kaamba kosowa kwa uphungu oyenera komanso thandizo la zaumoyo mwazina.

Pozindikiranso kuti bomali, lili mkati molimba ndi mavuto ngati awa, Ife a Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC, sitinakhale chete, lero pa 26 July, tikhala tili pa Juma, Mumba ndi Kaning'a, m'manisipalite ya Kasungu, ufalitsa uthenga wa zaumoyo kwa achinyamata komanso upereka thandizo lomwe lingateteze pa nthawi yomwe ali pa holideyi.

Tiyeni tikumane kumeneku, kuyambira nthawi ya 1 koloko masana.

Ministry Of Health - Malawi Development Network for Youth Empowerment - Deneye Malawi Government Kasungu District Council IM Swedish Development Partner Southern Africa Banja La Mtsogolo Youth Wave Malawi

-Youth Corner
No One Behind

Mkulu woyang'anira achinyamata pa nkhani zaumoyo wa ubereki ndi ufulu okhudza kugonana m'boma la Kasungu, Esnai Zimba, w...
23/07/2026

Mkulu woyang'anira achinyamata pa nkhani zaumoyo wa ubereki ndi ufulu okhudza kugonana m'boma la Kasungu, Esnai Zimba, wati ndi okondwa kaamba khwimbi la achinyamata omwe anabwera kudzalandira thandizo la zaumoyo monga kuyezetsa magazi, matenda opatsirana pogonana, kutenga njira zakulera komanso uphungu wa zaumoyo kwa Mtondo m'dera la Kasungu Manisipalite ya m'bomali.

Malinga ndi Zimba, ntchitoyi ndi gawo limodzi lothana ndi mavuto omwe akuta achinyamata m'bomali, monga kutenga pathupi kwa atsikana akadali achichepere komanso matenda opatsirana pogonana mwazina.

Mbali ina a Zimba ati akhala akufalitsa uthengawu komanso kupereka thandizoli kwa achinyamata onse m'madera osiyanasiyana m'bomali.

M'mawu ake, Village Head Chipuka wayamika azaumoyo chifukwa chopititsa thandizo la zaumoyo m'deralo, ponena kuti lithandiza achinyamata ambiri kupeza mpumulo ku mavuto omwe akumana nawo pa miyoyo yawo.

Ntchitoyi, yomwe inakonzedwa ndi gulu la achinyamata a Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC, ikhala ikupitirira Lamulungu likudzali pa 26 mwezi uno m'manisipaliteyi, kudzera mu ma (road shows).

Ministry Of Health - Malawi Malawi Government Kasungu District Council Youth Wave Malawi Family Planning Association of Malawi IM Swedish Development Partner Southern Africa Plan International Girls on the lead young feminist movement Girls on the Run International Development Network for Youth Empowerment - Deneye

-Youth Corner
No One Behind

Awa ndi ena mwa anamwino komanso azamba a pa chipatala chachikulu cha m'boma la Kasungu. Aliyese mwa iwowa, ali ndi mbir...
21/07/2026

Awa ndi ena mwa anamwino komanso azamba a pa chipatala chachikulu cha m'boma la Kasungu.

Aliyese mwa iwowa, ali ndi mbiri ya ulendo wake kuti afike apa, ena ankayenda mtunda wautali popita ku sukulu, ena ankasowa ngakhale chakudya, ndalama ya fizi komanso kuchitilidwa nkhaza ndi anzawo (tizi) mwazina.

Komabe, m'malo moyang'ana zopinga kapena kubwerera m'mbuyo, iwo anayika maso awo patsogolo ndipo lero ndi awa anakwanilitsa maloto awo ndipo pano akugwira ntchito yothandiza miyoyo ya anthu usana ndi usiku m'bomali.

Izi zikutikumbutsa komanso kutipatsa mangolomera kuti ulendo ukhoza kukhala wovuta, koma sukuyenera kutilepheretsa zomwe timafuna titafikira. Kwa inu ophunzira komaso makolo omwe pakadali pano mukuyesetsa kuthandiza ana anu kuti pa m'mawa adzakhale pabwino, musataye mtima kapena chiyembekezo chilimikanibe.

Poliza, tiyeni tiwanyadire ndi kuwafunira zabwino zonse, ogwira ntchito zaumoyo m'bomali pomwe akupitiriza kugwira ntchito yawo mwa ukadaulo.

Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC Ministry Of Health - Malawi IM Swedish Development Partner Southern Africa Youth Wave Malawi Kasungu District Council Banja La Mtsogolo Girls on the lead young feminist movement Family Planning Association of Malawi

-Youth Corner
No One Behind

  Lero pa 19 July, 2026, Ife a Kasungu District Hospital Youth Corner, timayembekeza kukhala ndi chipatala cha achinyama...
19/07/2026



Lero pa 19 July, 2026, Ife a Kasungu District Hospital Youth Corner, timayembekeza kukhala ndi chipatala cha achinyamata kwa Mtondo, m'manisipalite ya m'boma la Kasungu, koma sizinatheke kaamba ka zovuta zina, m'malo mwake, tikuyembekeza ukhala nacho lachinayi pa 23 mwezi omwe uno.

Komabe, ngakhale kuti izi zili chomwechi, mawa lolemba pa 20, tikhala tili kwa Suza m'bomali, ufalitsa uthenga okhudza uchembere wabwino limodzi ndi akulu-akulu azaumoyo m'bomali ndi cholinga chofuna kuchepetsa imfa za amayi ndi makanda zoodza kaamba ka ubereki.

Tiyeni tigwirane manja popitsita patsogolo ntchito zaumoyo m'bomali.

Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC Ministry Of Health - Malawi Family Planning Association of Malawi IM Swedish Development Partner Southern Africa Malawi Government Kasungu District Council Youth Wave Malawi Girls on the lead young feminist movement

-Youth Corner
No One Behind

Azaumoyo m'boma la Kasungu ati kusowa kwa uthenga oyenera pa nkhani ya ubereki wabwino kukupitiriza kuyika pa chiopsezo ...
17/07/2026

Azaumoyo m'boma la Kasungu ati kusowa kwa uthenga oyenera pa nkhani ya ubereki wabwino kukupitiriza kuyika pa chiopsezo miyoyo ya amayi oyembekezera ndi makanda m'madera osiyanasiyana m'bomali.

Mkulu woona za umoyo wa amayi ndi ana, Baziwell Malisen, wanena izi kwa Yamwa m'dera la mfumu yayikulu Wimbe ku Kasungu, pomwe amafalitsa uthenga wokhudza kufunika koyamba sikelo mwamsanga, kuyezetsa khansa ya khomo la chiberekero komanso kugwiritsa ntchito njira zakulera.

A Malisen ati mavutowa akukula kwambiri m'madera a Suza, Chisazima, Chitekwe ndi Wimbe, kotero apempha anthu kuthamangira kuchipatala kukalandira uphungu ndi thandizo la zaumoyo pa nthawi yake kuti achepetse imfa za amayi ndi makanda.

M'mawu ake, mfumu Yamwala yati ipitiliza kulimbikitsa anthu m'deralo kutsatira uthenga wa zaumoyo ndi cholinga choti anthu akhale ndi umoyo wathanzi.

Kudzera mu zisudzo za achinyamata a Kasungu komanso mwayi opereka mafunso, anthu ambiri alandira uthenga okhudza ubereki wabwino.

Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC Ministry Of Health - Malawi IM Swedish Development Partner Southern Africa Malawi Government Kasungu District Council Girls Empowerment Network Youth Wave Malawi Girls on the lead young feminist movement

-Youth Corner
No One Behind

Address

P/Bag 19
Kasungu

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Kasungu District Hospital Youth Corner - KDHYC posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share